Kumwalila kwa Lazalo
1 Padali ni mundhu mmojhi wa ku Besania, wamatanidwa Lazalo, wamadwala. Wamakhala kuchijhijhi cha Besania kumeneko amakhala ni achalongo wake Malia ni Masa. 2 Malia uyu nde yujha wadaanyeka Ambuye mafuta ya mtengo wa ukulu yayo yanunghila ni kuichangula myendo kwa machichi yake. Mbale wake Lazalo nde uyo wadali odwala. 3 Chimwecho achalongo wake Lazalo onjhe adatuma uthenga kwa Yesu, "Ambuye mmbwenji lanu wadwala!"
4 Yesu yapo wadavela chimwecho, wadakamba, "Lazalo siwamwalila kwa utenda uno, nambho wadwala ndande ya kwaapacha Amnungu ulemelelo, wadwala dala Mwana wa Amnungu walemekezedwe kupitila utenda umeneo."
5 Yesu wadali ni ubwenji wa pamtima ni Masa ni Malia ni Lazalo. 6 Yapo wadavela kuti Lazalo wadwala, Yesu wadaendekela kukhala pamalo pajha wadali kwa masiku yawili. 7 Ndiipo pambuyo pa yameneyo, wadakambila oyaluzidwa wake, "Chipano tiyeni tibwelenjho ku Yudea!"
8 Oyaluzidwa wake adamkambila, "Oyaluza! Yapita ndhawi yo chepa Ayahudi yapo amafuna kuiiphani kwa myala, ndande yanji mfuna kupitanjho kumeneko?"
9 Yesu wadayangha, "Bwanji saa za usana osati khumi ni ziwili? Chimwecho mundhu akayenda usana siakhoza kujhikhuwala ndande aliona dangalila la jhiko lino. 10 Nambho usiku mundhu wajhikwala ndande dangalila palibemo mkati mwake." 11 Yesu yapo wadakamba mawu yameneyo, wadaakambila, "Mbwenji lathu Lazalo waghona litulo, nambho ine sinipite kumuucha."
12 Oyaluzidwa wake adamkaambila, "Ambuye ngati waghona, siwauke."
13 Anyiiwo amaghaniza wamakamba kuti waghona litulo, nambho wamakambilila nyifa ya Lazalo. 14 Ndiipo, Yesu wadakambila popande kwa bisa, "Lazalo wamwalila,