Pular para o conteúdo
Publicidade

João 12

Yesu walowa ku Yelusalemu kokondwa

12 Mawa lake gulu lalikulu la wandhu anyiyao adajha ku pwando la Pasaka, adavela kuti Yesu wali mnjila kujha ku Yelusalemu. 13 Ndiipo adatenga ndhawi za zing’onozingono za mitengo ya mitende, ni kupita kumlandila, adakweza mvekelo ni kukamba, "Uelekelo! Wapachidwe mwawi uyo wakujha kwa jhina la Ambuye. Wapachidwe mwawi Mfumu wa Izilaeli!"

14 Ndiipo Yesu wadamwona mwana wa phunda, wadakhala pamsana pake ngati umo yakambila malembo.

15 "Simudaopa wandhu a ku Yelusalemu!

Vechelani, Mfumu wanu watokujha,

Wakwela mwana wa phunda!"

16 Vindhu vimenevo oyaluzidwa wake samavijhiwe kuyambila mmayambo, Yesu yapo wadapachidwa ulemelelo, nde yapo adakumbukila kuti wadalembedwela yameneyo, ni wandhu amchitila iye.

17 Wandhu anyiyao adalipo ndhawi iyo Yesu wamamtana Lazalo kuchokela kuchiliza, ni kumuhyucha, adamchochela umboni. 18 Chimwecho gulu limenelo la wandhu lidamlandila, mate yake onjhe adavela kuti Yesu wadachita chizindikilo chimenecho. 19 Ndiipo Afalisayo adakambilana, "Mvela? Sitikhoza kuchita kandhu! Penyani jhiko lonjhe la panjhi limchota iye."

Veja também