23 Pampajha wadatulukila mundhu wachiwanda mujha mnyumba yokomanilana Ayahudi, wadakweza mvekelo waukulu, 24 "Ufuna kutichita chiyani iwe Yesu wa ku Nazaleti? Bwanji, wajha kutipha? Ine nijhiwa kuti iwe ni Woyela, kuchokela kwa Mnungu!" 25 Yesu wadachinyindila chiwanda, "Khala chete! Mchoke mundhu uyu." 26 Chiwanda chimenecho chidamtingiza kwa mbhavu mundhu yujha, chidalila kwa mvekelo waukulu, ni kumchoka.