Yesu waachuka myendo oyaluzidwa wake
1 Yapo lidawandikila siku la pwando la Pasaka, Yesu wadajhiwa kuti ndhawi yake yochoka pajhiko lapanjhi ni kupita kwa Atate ya kwana. Kila ndhawi wadaakonda wandhu wake anyiyao ali pajhiko, chimwecho wadaakonda mbaka kuuchocha umoyo wake!
2 Yesu wadali ni oyaluzidwa wake adakhala kudyaa chakudya cha ujhulo. Satana wadathomthila Yuda, mwana wa Simoni, mtima wa kumng’anamuka Yesu. 3 Yesu uku ni wajhiwa kuti Atate ampacha kila kandhu muulamulilo wake, ni kuti wadachoka kwa Amnungu ni kubwela kwa Amnungu. 4 Ndiipo, wadasiya kudya chakudya, wadavula njhalu yake ya kubwalo, wadatenga chitambaa chochangulila ni kujhimanga muchiuno. 5 Ndiipo Yesu wadapungulila majhi mbeseni ni kuyamba kwa kwasambiza oyaluzidwa wake mmyendo ni kwachangula kwa chitambaa icho wadajhimanga. 6 Chimwecho yapo wadafika kwa Petulo, Petulo wadafunjha, "Ambuye simunichuke niine mmyendo?"
7 Ndiipo Yesu wadayangha, "Siuchijhiwa icho nichita chipano, nambho pambuyo siujhiwe."
8 Petulo wadamkambila, "Siunichuka myendo muyaya!"
Yesu wadayangha, "Nikasia kukuchuka siukhalanjho ni mgwilizano ni ine."
9 Simoni Petulo wadamkambila, "Ambuye, nichukeni, osati mmyendo pe nambho ni manja ni mutu wanga."
10 Yesu waadakambila, "Mundhu wakathosamba mthupi walibe haja yosambanjho, nambho wafunika kusamba mmyendo, ndande wathoyela thupi lonjhe. Anyiimwe mwayela, nambho osati mwaonjhe." 11 Yesu wadamjhiwa uyo siwamng’anamuke, nde ndande wadakamba, "Anyiimwe mwayela, nambho osati mwaonjhe."
12 Yapo wadathokwasambiza mmyendo ni kuvalanjho njhalu yake ni kukhalanjho pachakudya, wadaafunjha, "Bwanji, mwayajhiwa yayo nakuchitilani? 13 Anyiimwe munitana Oyaluza ni Ambuye, mwakamba mwauzene ine nde mmeneyo. 14 Chipano, ngati ine nili Ambuye ni Oyaluza wanu, nakuchukani anyiimwe myendo, namwe ifunika muchukane myendo. 15 Nakupachani chifani kuti namwe mchite ngati umo nachitilani ine. 16 Zenedi nikukambilani, mbowa osati wamkulu kumpitilila wamkulu wake, ni mtumwi osati wamkulu kusiyana ni uyo wamtuma. 17 Chipano, ndande mwayajhiwa yaya, Amnungu siakupacheni mwawi mkayachita."