Pular para o conteúdo
Publicidade

João 21

Yesu waachokela oyaluzidwa saba

1 Pambuyo pa yameneyo, Yesu wadaachokela oyaluzidwa wake muchijha la nyanja Tibelia. Wadaachokela chimwechi. 2 Simoni Petulo, Tomaso uyo wamatanidwa Mawila, Nasanaeli mundhu wa ku Kana ya Galilaya, wana awili a Zebedayo ni oyaluzidwa wake wina awili, adali onjhe pamojhi.

3 Simoni Petulo wadaakambila achaanjake, "Nipita kuvuwa njhomba."

Nao adaamkambila, "Tipita taonjhe kuvuwa." Ndiipo adapita, adakwela mbwato, nambho usiku umeneo sadapate kandhu. 4 Malenga kucha, Yesu wadaima mbhepete mwa nyanja, nambho oyaluzidwa sadajhiwe kuti nde Yesu. 5 Ndiipo, Yesu wadaafunjha, "Anyamata wanga, simudapate njhomba yaliyonjhe?"

Adayangha, "Sitidapate kandhu."

6 Yesu wadaakambila, "Chichani khokha bendeka lakwene la bwato simupate njhomba." Ndiipo adaponya khokha bendeka limwelo nambho adalepela kuguza ndande ya kuchuluka kwa njhomba.

7 Chimwecho yujha oyaluzidwa wamakondedwa kupunda ni Yesu, wadamkambila Petulo, "Ekee Ambuye!" Simoni Petulo yapo wadavela kuti Ambuye, wadavala njhalu yake, ndande siwadavale njhalu, ni kujhitaya mmajhi. 8 Nambho anyiwajha oyaluzidwa wina yawo adali pamtunda, adajha pa bwato uku niaguza khokha lojhala njhomba, adali ngati utali mita mia kuchoka pamtunda. 9 Yapo adafika pamtunda adapheza moto wa makala wasonghedwa, njhomba niziochedwa ni bumunda. 10 Yesu wadaakambila, "Majhanazoni njhomba zakumojhi izo mwavuwa."

11 Chimwecho, Simoni Petulo wadakwela mubwato, wadaguza khokha limenelo mbaka kumtunda lidajhala njhomba zazikulu mia imojhi ni hamsi ni zitatu. Atangati njhomba zidachuluka, sizidang’ambe khokha.

Veja também