Pular para o conteúdo
Publicidade

Yohana 1

45 Filipo yapo wadampheza Nasanaeli, wadamkambila, "Tampheza uyo Musa wadalemba nghani zake muchikalakala cha Thauko, ni uyo alosi adalemba nghani zake, ndekuti Yesu mwana wa Yusufu wa ku Nazaleti."

46 Nasanaeli nayonjho wadamfunjha Filipo, "Bwanji, chindhu cha bwino chikhoza kuchokela ku Nazaleti?"

Ndiipo Filipo wadayangha, "Majha uone."

47 Yesu yapo wadamuona Nasanaeli niwajha kwake, wadakamba nghani zake, "Mmeneyo Muizilaeli mwene. Palibe choipa mkati mwake."

48 Nasanaeli nayonjho wadamfunjha, "Waniona bwanji?"

Yesu wadayangha, "Yapo udali panjhi pa mtengo wa mtini, Filipo wakali osakutane, nidakuona."

49 Ndiipo Nasanaeli wadamkambila, "Oyaluza, imwe ni Mwana wa Amnungu. Imwe ni Amfumu a ku Izilaeli!"

50 Ndiipo Yesu wadafunjha, "Wakhulupilila ndande nakukambila kuti nakuona panjhi pa mtengo wa Mtini? Siuvione vindhu vavikulu kupunda kupitilila ivi." 51 Yesu wadaendekela kukamba, "Nikukambilani uzene, simuone kumwamba nikuvunukuka niatumiki akumwamba Amnungu ni akwela ni kuchika pamwamba pa Mwana wa Amnungu."

Veja também