23 Asikali adampachika Yesu, adazitenga njhalu zake, adazighawa malundo yanai, kila asikali lundo limojhi. Adatenga njhalu yake yaitali iyo idasokedwa chipande chimojhi, popande msoko. 24 Asikali adakambilana, "Njhalui tisadaing’amba, nambho tibule kula siikhale ya yani." Chindhu ichi chidachitika dala yakwanile malembo yo yela yakamba,
"Adaghawana vivalo vanga,
Njhalu yanga aibulila kula."
Chimwecho nde umo adachitila asikali ameneo.
25 Pafupi ni mtanda wa Yesu adaima amaye wake, akulu wao wa amake, Malia wamkazi wa Kileopa, ni Malia uyo wadachokela kumujhi wa Magidala. 26 Yesu yapo wadaona amake aima pafupi ni oyaluzidwa uyo wamamkonda, wadaakambila amaye wake, "Maye! Mwana wanu uyo yapo."
27 Ndiipo wadamkambila yujha oyaluzidwa wake Yohana, "Amaye wako yawo yapo." Kuyambila ndhawi imeneyo oyaluzidwayo wadatengedwa ni amaye wake Ayesu kukhala kukhomo kwao.