Yesu wamlamicha mundhu wovuwala Siku lo Pumulila
1 Pambuyo pa yameneyo kudalipo ni phwando la Ayahudi, nayo Yesu wadapita Ku Yelusalemu. 2 Kumeneko ku Yelusalemu, pafupi ni chicheko icho chitanidwa chicheko cha mbelele, kudaliko ni thiwi ilo kwa mkambo wa Chihebulaniya, Betizata, ilo lidazungulilidwa ni khumbi zisano. 3 Mkati mwake mudali odwala ambili, osapenya, andendele, ni ovuwala. Amalindilila majhi yavundulidwe, 4 pakuti ndhawi za mbili mtumiki wa kumwamba wa Amnungu wamachika ndhawi zina ni kuyavundula majhi. Mundhu waliyonjhe uyo wachogolela kubila mmajhi yayo yamavundulidwa, wamalama ndhenda yaliyonjhe iyo wamadwala. 5 Ndiipo, pamwepo wadalipo mundhu mmojhi uyo wadali odwala kwa ndhawi ya vyaka selasini ni nane. 6 Yesu yapo wadamuona mundhu mmeneyo wagona pamenepo ni kujhiwa kuti wadakhala kwa ndhawi ya itali, wadamfunjha, "Bwanji, ufuna kulama?"
7 Nayo wadayangha, "Wakulu, ine nilibe mundhu onibiza mthiwi majhi yapo yavundulidwa. Yapo niyesa kulowa, mundhu mwina wanichogolela."
8 Yesu wadamkambila, "Ima tenga chika lako ujhiyenda." 9 Pampajha mundhu mmeneyo wadalama, wadatenga chika lake ni kuyamba kuyenda.
Chindhu ichi chidachitika Siku lo Pumulila.