21 Ngati umo Atate wahyukicha omwalila ni kwapacha umoyo, chimwecho Mwana wapacha umoyo yao wakonda. 22 Atate siamulamula mundhu waliyonjhe, njhito yonjhe yo lamula wamsiila Mwana, 23 kuti wandhu wonjhe amlemekeze Mwana ngati umo walemekezela Atate. Waliyonjhe uyo siwamlemekeza Mwana siwalemekeza yao amtuma."
24 "Zene nikukambilani, mundhu waliyonjhe uyo wavela mawu yanga ni kwaakhulupilila Amnungu yawo anituma, ali ni umoyo wa muyaya. Sialamulidwa muyaya, nambho wachoka kunyifa ni kulowa kuumoyo. 25 Zene nikukambilani, ndhawi ikujha ni chipano ilipo, yapo omwalila savele mvekelo wa Mwana wa Amnungu, ni anyiyao savele mvekelo saakhale ni umoyo. 26 Ngati umo Atate ali chiyambo cha umoyo, chimwecho ampacha Mwana wao kukhala chiyambo cha umoyo. 27 Chimwecho ampacha ulamuli olanga ndande iye ni mundhu Amnungu watuma. 28 Simudadabwa chindhu ichi, mate yake ndhawi ikujha yapo onjhe anyiyawo ali mviliza savele mvekelo wake, 29 onjhe sahyuke, anyiyawo achita vabwino sahyuke ni kupata umoyo wa muyaya, ni anyiwajha achita voipa sahyuke ni kulangidwa."
Anyiwajha akamba nghani za Yesu
30 "Ine sinikhoza kuchita chindhu kwa mbhavu zanga namwene. Ine ni lamula ngati umo nivelela kuchoka kwa Atate, ni lamulo langa ni lo vomelezeka. Pakuti sinifuna kuchita chikondi changa namwene, nambho umo wakondela uyo wanituma."
31 "Ngati nikajhichochela umboni namwene, umboni wanga siukhoza kuvomeleka kuti wa uzene.