66 Ndhawi imweyo, ochatila ambili pakati pao adamsiya, siadachogozane nayenjho. 67 Ndiipo, Yesu wadaafunjha ochatila khumi ni awili, "Anyiimwe namwe mfuna kuchoka?"
68 Simoni Petulo wadamyangha, "Ambuye tipite kwa yani? Akati imwe muli ni mawu ya umoyo wa muyaya. 69 Ife tikhulupilila, ni tijhiwa kuti imwe nde yujha Oyela Amnungu"