4 Ndiipo adamfunjha Yesu, "Oyaluza, wamkazi uyu wagwilidwa ni wachita chigololo. 5 Muthauko, Musa wadatilamula wamkazi ngati uyu wabulidwe miyala mpaka kumwalila. Imwe mkamba bwanji?" 6 Adamuyesa kokamba chimwecho, kuti ampache mlandu. Nambho Yesu wadakwatama panjhi ni kulemba pa ndhaka kwa chala chake.
7 Yapo adapunda kumfunjha, wadaima nikwakambila, "Mundhu waliyonjhe uyo walibe machimo pakati panu wakhale oyamba kumbula mwala." 8 Wadakwatamanjho ni kulemba pandhaka kwa chala chake. 9 Yapo adavela chimwecho adayamba kuchoka mmojhimmojhi, adachogola azee. Wadakhalila Yesu yokha ni wamkazi waima pachogolo pake. 10 Yesu yapo wadaima wadamfunjha wamkaziyo, "Alikuti wajha wandhu akupacha mlandhu? Palibe waliyonjhe uyo wakulamula?"
11 Wamkazi mmeneyo wadayangha, "Wakulu, palibe waliyonjhe!"
Ndiipo Yesu wadamkambila, "Ata ine sinikulamula. Mapita siudachitanjho machimo."