33 Yapo adafika pamalo yapo patanidwa Fuvu la Mutu, kumalo kumeneko adampachika Yesu pamojhi ni wandhu wajha owananga. Mmojhi kwene ni mnjake kumanjele. 34 Yesu wadakamba, "Atate, mwalekelele wandhuwa, pakuti sajhiwa icho achichita." Ndiipo adagawana njhalu zake kwa kuchita gudugudu. 35 Wandhu adangoimilila pampajha naampenya. Ni achogoleli Ayahudi adamkwiicha Yesu pokamba, "Wadaombola wina! Chipano wajiombole mwene wake, ngatidi ni iye ni Kilisito, wosanghidwa ni Mnungu!" 36 Asikali nawo adaja, adamkwiicha, adampelekela divai yowawa, 37 Niayiiwo adamkambila, "Ngati zenedi iwe ni Fumu wa Ayahudi jhiombole umwene."
38 Chibao chidali pamwamba pa mtanda wake chidalembedwa chimwechi, UYU NDE FUMU WA AYAHUDI.
39 Mmojhi wa wajha owananga adapachikidwa mmitanda pamojhi ni Yesu wadamtukwana, niwakamba, "Bwanji, iwe sinde Kilisito uyo wasanghidwa ni Mnungu? Jhiombole mwene utiombole ni ife." 40 Nambho owananga mnjake wadamnyindila, wadakamba, "Bwanji, iwe suopa Mnungu ata pang’ono? Pakuti iwe nawe wapachikidwa ngati iye. 41 Iwe ni ine tafunika yaya, ndande yaya nde mkokolo wa volakwa vathu. Nambho mundhu uyu siwadachite cholakwa chilichonjhe." 42 Ndiipo yujha owananga wadamkambila Yesu, "Imwe Ayesu! Mnikumbukile yapo simulowe mu Ufumu wanu." 43 Yesu wadamuyangha, "Nikukambila uzene, lelolino siukale pamojhi ni ine kumwamba."