40 Nambho owananga mnjake wadamnyindila, wadakamba, "Bwanji, iwe suopa Mnungu ata pang’ono? Pakuti iwe nawe wapachikidwa ngati iye. 41 Iwe ni ine tafunika yaya, ndande yaya nde mkokolo wa volakwa vathu. Nambho mundhu uyu siwadachite cholakwa chilichonjhe." 42 Ndiipo yujha owananga wadamkambila Yesu, "Imwe Ayesu! Mnikumbukile yapo simulowe mu Ufumu wanu." 43 Yesu wadamuyangha, "Nikukambila uzene, lelolino siukale pamojhi ni ine kumwamba."