Pular para o conteúdo
Publicidade

Mateus 18

Mbale wako yapo wachita machimo

15 "Ngati mbale wako wakalakwila, mchate umkambile kulakwa kwake muli awilipe. Wakakuvela siikhale wampata mbale wako. 16 Nambho ngati siwakane kukuvela, funa mundhu mwina mmojhi kapina awili pamojhi ni iwe, kuti mau lililonjhe lichimikizike kwa amboni awili kapina atatu ili mavuto yathele, ngati umo yalembedwa mmalembo. 17 Ngati siwakane kwaavela achamenewo, ukambile mpingo, ngati siwakane kuuvela mpingo, basi mchite mundhu mmeneyo ngati mundhu uyo siwamjhiwa Mungu kapima wolandila nsongho."

Kukaniza ni kuloleza

18 "Zene ikukambilani, yayo simuyamange pajhiko la panjhi chinchijha siyamangidwe kumwamba, ni icho simuchimasule pajhiko la panjhi chinchijha sichimasulidwe kumwamba.

19 "Zene nikukambilani, awili pakati panu akavomelezana pajhiko la panjhi kuusu chilichonjhe icho afuna kupembha, Atate wanga a kumwamba siakuchitileni. 20 Pakuti yapo asonghana wandhu awili kapina atatu kwa jhina langa, ine nili pamojhi nao."

Veja também