Maye wa Yakobo ni Yohana wampembha Yesu chindhu
20 Ndiipo, maye wa wana a Zebedayo pamojhi ni wana wake adajha kwa Yesu, wadagwada pachogolo pake ni kumpembha wamchitile icho wachifuna.
21 Yesu wadamfunjha, "Ufuna chiyani?"
Wamkazi yujha wadakamba, "Chonde nikambile uzene, wana wanga awiliwa akhale mmojhi ku jhanja la manjele ni mwina ku jhanja la kwene ku Ufumu wako."
22 Yesu wadaakambila, "Simujhiwa icho mupembha, bwanji, mukhoza kumwela chikho cha mavuto ngati icho sinimwele ine?"
Anyiiwo adamuyangha, "Tikhoza,"
23 Yesu wadaakambila, "Zene simchimwele chikho cha mavuto ngati umo sinichimwele ine, nambho nilibe lamulo yosangha yani wakhale ku manjele kwanga kapina kwene kwanga. Malo yameneyo yaikidwa ndande ya anyiwajha asanghidwa ni Atate wanga."