Yesu waalamicha osapenya awili
27 Yesu yapo wamachoka pamalo pamenepo, yapo wadali mnjila, osapenya awili adamchata, adakamba, "Mwana wa Daudi, utilengele lisungu!"
28 Yesu yapo wadalowa mnyumba, wajha osapenya awili adamchata, wadaafunjha, "Bwanji, mkhulupilila kuti nikhoza kukulamichani?"
Anyiiwo adamuyangha, "Yetu, Ambuye."
29 Yesu wadaagafya maso yao, wadakamba, "Ikhale chimwecho ngati umo mukhulupilila." 30 Maso yao yadakhoza kupenya. Yesu wadakaniza kupunda, "Msadamkambila mundhu waliyonjhe vindhu ivi!"
31 Nambho anyiiwo adachoka, adaeneza nghani za Yesu mujhiko lonjhe lijha.