Ukwati mmujhi wa Kana
1 Siku la katatu kudali ni ukwati mmujhi wa Kana, mkoa wa ku Galilaya, nawo amaye wake Yesu adalipo pamwepo, 2 Yesu naye wadalalikidwa pa ukwati pamojhi ni oyaluzidwa wake. 3 Divai yapo idatha, amaye wake adamkambila Yesu, "Divai yatha."
4 Ndiipo Yesu wadayangha amaye wake, "Ndandeyanji munikambila nghani imeneyo. Ndhawi yochita njhito yanga ikali yosafika."
5 Chimwecho amake adazikambila mbowa, "Chilichonjhe icho siwakukambileni, chitani,"
6 Pamenepo padali ni mapipa sita ya myala, iyo yaikidwa kwa chikhalidwe chakusamba cha Chiyahudi, kila mchuko udakakhoza kutenga michuko ya wili kapina itatu ya majhi. 7 Ndiipo Yesu wadaakambila, "Jhazani majhi mmapipa." 8 Ndiipo wadaakambilanjho, "Chipano tungani mkampelekele wamkulu wa phwando." 9 Wamkulu waphwando yapo wadalawa majhi yameneyo, wadapeza yang’anamuka kukhala divai. Siwada jhiwe uko ya choka, nambho anyiyawo adatunga majhi adajhiwa. Wamkulu wa phwando wadamtana wammuna wa ukwati, 10 wadamkambila, "Kila mudhu wayamba kwapacha wandhu divai ya bwino uti, ni akathokumwa ni kukwana, wakonja ijha yosakome. Nambho iwe wachocha divai ya bwino mbaka saino."
11 Yesu wadachita chizindikilo ichi choyamba ku Kana, ya ku Galilaya wadaalangiza ulemelelo wake, ni oyaluzidwa wake adamkhulupilila.