Yesu wamtulukila Malia uyo wadachokela ku Magidala
11 Nambho Malia wadaima pabwalo pa chiliza, wamatolila. Yapo wamalila, wadakwatama ni kuzuzumila mchiliza, 12 wadaona atumiki akumwamba Amnungu awili avala njhalu zoyela mbee, akhala yapo lighonekedwa thupi la Yesu, mmojhi kumutu mwina kumyendo. 13 Atumiki akumwamba achameneo adamfunjha malia, "Maye, ndande yanji mulila?"
Wadamkambila, "Waachocha Ambuye wanga, sinijhiwa ukoaikidwa!"
14 Yapo wadakamba yameneyo, wadang’anamuka kumbuyo, wadamuona Yesu waima pamenepo, nambho siwadajhiwe kuti nde Yesu. 15 Yesu wadamfunjha, "Maye, ndande yanji mulila? Mumfunafuna yaani?"
Malia wamaganiza osunga busitani, wadamkambila, "Olemekezedwa ngati imwe nde mwaatenga, pepani nipembha munilangize ukomwamuika, sinimtenge."
16 Yesu wadamkambila, "Malia!"
Malia nayo wadang’anamuka, wadamkambila kwa Chihebulania, "Laboni" Mate yake "Oyaluza."
17 Yesu wadamkambila, "Usadanigwila, ndande nikali osapite kumwamba kwa Atate. Nambho mapita kwachabale wanga ukaakambile. Nipita kumwamba kwa Atate wanga ni Atate wanu, Amnungu wanga ni Amnungu wanu."
18 Chimwecho Malia uyo wadachokela ku Magidala wadapita kwaapacha nghani oyaluzidwa naona Ambuye, ni kuti wadamkambila chimwecho.