Yesu waapacha wandhu elufu zisano chakudya
1 Pambuyo pa yameneyo, Yesu wadayomboka nyanja ya Galilaya, iyo imatanidwanjho Tibelia. 2 Ndiipo Gulu lalikulu la wandhu lidaendekela kumchota ndande adaviona vizindikilo ivo wadachita pa kwalamicha odwala. 3 Ndiipo Yesu wadakwela kuphili, wadakhala pamojhi ni oyaluzidwa wake. 4 Ndhawi imeneyo phwando la Pasaka la Ayahudi lidawandikila. 5 Yesu yapo wadapenya ni kuona gulu lalikulu nilimjhela, wadamkambila Filipo, "Sitigule kuti mabumunda yakudya wandhu adye?" 6 Yesu wadakamba chimwecho kwa kumuyesa Filipo, pakuti wadajhiwa icho siwachichite.
7 Ndiipo Filipo wadamuyangha, "Ata ngati tidakhala ni ndalama zochuluka sizikwana kughula chakudya cha kwakwana wandhu anyiyawa, hata ngati kila mmojhi wasiwapachidwe chibandu chaching’onope"
8 Oyaluzidwa wake mwina uyo wamatanidwa Andulea, mbale wake wa Simoni Petulo, wadamkambila, 9 "Walipo mnyamata mmojhi uyo wali ni mabumunda yasano iyo yakonjedwa kwa ufa wa shayili ni njhomba ziwili, nambho vindhu ivi sivikwana kwa wandhu onjhewa?"
10 Ndiipo Yesu wadakamba, "Akambileni wandhu akhale panjhi." Pamalopo padali ni matengo yayafupiyafupi yambili. Ndiipo adakhala, adalipo wachimuna elufu zisano. 11 Chimwecho Yesu wadatenga mabumunda, wadaayamika Amnungu, wadagaawila wandhu anyiyao adakhala panjhi, kila mmojhi wadapata ngati umo wadafunila, wadachita chimwecho ni zijha njhomba. 12 Wandhu yapo adakhuta, Yesu wadaakambila oyaluzidwa wake, "Kusani vipande ivo va khala visadataika." 13 Chimwecho adakusa vipande vijha va mabumunda ni kuvitila mvitundu. Adavijhaza mvitundu kumi ni viwili.
14 Ndiipo wandhu anyiwajha yapo adaona vizindikilo ivo wadachita Yesu, adakamba, "Zenedi uyu nde mlosi uyo wakujha pa jhiko."