Pular para o conteúdo
Publicidade

Yohana 9

Yesu wamlamicha mundhu uyo wabadwa osapenya

1 Siku limojhi Yesu yapo wamapita wadamuona mundhu mmojhi, uyo siwapenya kuyambila kubadwa kwake. 2 Basi oyaluzidwa wake adamfunjha, "Oyaluza! Yani wachita machimo, mundhu uyu kapina obala wake, mbaka wabadwe osapenye?"

3 Yesu wadaayangha, "Wabadwa osapenye osati ndande ya machimo yake, kapina ya obala wake, wadabadwa chimwecho kuti mbhavu ya Amnungu iwoneke muumoyo wake. 4 Ifunika tiendekele kuzichita njhito za yawo atituma kukali usana, ndande usiku ukujha uwo mundhu waliyonjhe siwakhoza kuchita njhito. 5 Ndhawi nili pano pajhiko, ine nde dangalila la wandhu a pajhiko."

6 Yapo wadakamba chimwecho, wadalavula malovu panjhi, wadakonja thokope, wadamnyeka yujha osapenyeyo mmaso, 7 wadamkambila, "Pita ukasambe kuthiwi la Siloamu." Mawu Siloamu mate yake Uyo watumidwa. Chimwecho wadapita kusamba, wadabwela uku ni wapenya.

8 Ndiipo, apafupi wake ni wina yao amajhiwa kuti poyamba wadali osauka pembhapembha, adakamba, "Uyu osati osauka yujha wamakhala ni kupembha?"

9 Wina adakamba, "Ndemwene." Wina adakambanjho, "Notho! Wangolingana nayo."

Nambho yujha wadali osapenyayo wadakamba, "Nde ine!"

10 Basi amamfunjha, "Chipano, maso yako yakhoza bwanji kupenya?"

11 Wadayangha, "Yujha mundu watanidwa Yesu wadakonja thokope, wadaninyeka mmaso ni kunikambila nipite nikasambe ku thiwi la Siloamu. Pamenepo ine nidapita kusamba kumaso, pampajha nidakhoza kupenya."

12 Adamfunjha, "Iye walikuti?" Nayo wadaayangha,

"Ine sinijhiwa!"

Veja também