59 Yapo lidakwana siku la nane kuyambila kubadwa kwa mwana, adapita kumdula jhando, ni achabale wake amafuna kumpacha jhina la atate wake ilo limatanidwa, Zakaliya. 60 Nambho amake adakana, ni kukamba, "Notho! Watanidwe jhina Yohana." 61 Anyiiwo adamuyangha, "Palibe mundhu ata mmojhi pa khamu lako uyo wali ni jhina limenelo." 62 Ndiipo anyiiwo adaafunjha atate wake kwa vizindikilo kuti wakambe jhina ilo wafuna kumpacha mwana wake. 63 Iye wadatanicha chithabwa ni wadalemba chimwechi, "Jhina lake ni Yohana." Wandhu wonjhe adazizwa. 64 Ndhawi imweyo Zakaliya wadakhoza kukamba ni kumtamanda Mnungu.