Yesu wamulamicha mundhu wosapenya
35 Yapo Yesu wadali pafupi kufika ku Yeliko, wadakomana ni mundhu mmojhi wosapenya, uyo wadakhala mbhepete mwanjila kupembhapembha. 36 Yapo wadavela wandhu ambili niapita, wadafunjha, "Kuli chiyani?" 37 Adamuyangha, "Yesu wa ku Nazaleti watopita." 38 Ndiipo wosapenya mmeneyo wadakweza mvekelo, wadakamba, "Yesu Mwana wa Daudi, unilengele lisungu!" 39 Anyiwajha adali mchogolo adamnyindila kuti wakhale chete. Nambho iye wadaendekela kukweza mvekelo waukulu, "Mwana wa Daudi chonde, unilengele lisungu!" 40 Yesu wadaima ni kwalamula kuti ajhenayo kwaiye. Wosapenya yujha yapo wadafika pafupi, Yesu wadafumnjha, 41 "Ufuna nikuchitile chiyani?" Iye wadayangha, "Ambuye nifuna nikhoze kupenya." 42 Yesu wadamuyangha, "Penya, chikhulupililo chako chakulamicha." 43 Pampajha mundhu yujha wadakhoza kupenya, wadamchata Yesu uku niwamkweza Mnungu. Yapo adaona chimwecho, wandhu wonjhe adamtamanda Mnungu.