Yesu walowa mu Yelusalemu kwa chikondwelo
28 Yesu yapo wadamaliza kukamba chimwechio, wadachogolela kupita ku Yelusalemu. 29 Yapo wadawandikila ku mijhi ya Besifage ni Besania, pafupi ni phili ilo litanidwa phili la Mizetuni, wadatuma woyaluzidwa wake awili pakati pa oyaluzidwa wake, wadakambila, 30 "Mpite mmujhi uwo uli mchogolo mwanu. Yapo simulowe mmenemo, simumpheze phunda uyo siwadatumike ni mundhu waliyonjhe, wamangidwa mmasuleni mjhe nayo pano. 31 Mundhu uyo siwakufunjheni ndande yanji mummasula phunda, mkambileni, amfuna Ambuye."
32 Ndiipo adapita ni adakomana ngati umo adakambilidwa ni Yesu. 33 Yapo amammasula phunda yujha, mwene phunda wadaafunjha, "Ndande yanji mummasula phunda?" 34 Anyiiwo adayangha, "Ambuye amfuna." 35 Ndiipo, adampeleka kwa Yesu phunda yujha. Adayala njhalu pamwamba phunda ni kumkweza Yesu pamwamba pake. 36 Yapo wamaendekela ni ulendo, wandhu adayala njhalu zao panjila.
37 Yapo wadawandikila ku Yelusalemu, pa njila iyo ichikila pa phili la mizeituni, gulu lonjhe la wochatila wake adayamba kukondwela ni kumtamanda Mnungu pokweza mvekelo ndande ya vodabwicha vonjhe ivo adavionapo. 38 Adakamba, "Wali ni mwawi Mfumu uyo wakujha mu jhina la Ambuye. Mtendele ukhale kumwamba kwa Mnungu, ni ulemelelo kumeneko kumwamba kupunda!" 39 Afalisayo wina yawo adali mkati mwa gulu lijha, yapo adaona chimwecho, adamkambila Yesu, "Oyaluza, anyindileni oyaluzidwa wanu akhale chete!" 40 Yesu wadayangha, "Nikukambilani kuti, ngati anyiyawa saakhale chete, miyala siibule phokoso."