15 Yapo atumiki akumwamba a Mnungu adaasiya ni kupita kumwamba, owesa wajha adakambilana, adakamba, "Tiyeni ku Beselehemu tikaone icho chachokela, icho takambilidwa ni Ambuye."
16 Chimwecho, adapita msangamsanga ni kumkomana Maliya ni Yusufu, ni mwana wakhanda, uyo wadagonekedwa mchidiku cha sepedwa ndande yo dyechela Ng’ombe. 17 Owesa wajha yapo adamuona mwanayo, adauzila wandhu wina nghani za mwana mmeneyo izo adakambilidwa ni atumiki akumwamba kuhusu mwana. 18 Ni wandhu wonjhe yawo adavela nghani za mwana zo amakamba owesa zinyama adazizwa kupunda.