Pular para o conteúdo
Publicidade

Lucas 7

Chikhulupililo cha wamkulu wa asilikali wa Loma.

1 Yesu yapo wadamaliza kwakambila wandhu mawu yameneyo, wadachoka kupita ku Kapenaumu. 2 Kumeneko kudali wamkulu wa gulu la asilikali mwina uyo wadali ni mbowa wake uyo wamamkonda kupunda. Mbowa mmeneyu wadali wodwala pafupi kumwalila. 3 Wamkulu wa asilikali yujha yapo wadavela nghani za Yesu, wadaatuma azee wina wa Ayahudi, apite akampemphe kuti wamlamiche mbowa wake. 4 Yapo adafika kwa Yesu, adampempha kupunda, pokamba, "Mundhu uyu wafunikadi wathangatilidwe, 5 pakuti walikonda jhiko latu, ni iye watimangila, nyumba yopezanilana." 6 Ndiipo, Yesu wadapita pamojhi naanyaiwo. Yapo adawandikila kufika pakhomo pa yujha wamkulu wa asilikali, wamkulu wa gulu la asilikali wadaatuma achabwenji wake kwaiye amkambile, "Ambuye, msadajhichaucha kupunda, ndande ine siniloledwa kukulovyani imwe mnyumba mwanga. 7 Ndendande sinidajhione kuti ine nikhoza kujha kwanu imwe. Nambho kambani mawupe, ni mbowa wanga siwalame. 8 Pakuti inenjho ni mundhu uyo nili panjhi pa lamulo, ni nili ni asilikali panjhi panga, yao avela icho naakambila. Nikamkambila mmojhi, Pita,iye wapita. Ni wina nimutana, Majha,Nayonjho wakujha. Ni mbowa wanga nikamkambila, Chita chimwechi,nayonjho wachita."

9 Yesu yapo wadavela chimwechi wadazizwa, naye wadang’anamukila wandhu ambili yawo amamchata ni kwakambila, "Sinidaonepo chikhulupililo chachikulu ngati ichi ata pakati pa wandhu a Yelusalemu."

10 Wandhu wajha adatumidwa kwa Yesu, yapo adafika kukhomo kwa wamkulu wa asilikali adampheza mbowa wake watholama.

Veja também