24 Anyiwajha wandhu adatumidwa ni Yohana yapo adachoka, Yesu wadayamba kulikambila gulu la wandhu nghani za Yohana, niwakamba, "Bwanji, yapo mudapita kumuona Yohana kuphululu kujha, mudakhulupilila kuona chiyani? Bwanji, mdapita kuona bango nilitingizidwa ni mbhepo? 25 Bwanji, mudapita kuona chiyani? Bwanji, dapita kumuona mundhu uyo wavala njhalu za mtengo waukulu? Notho! Anyiyawo avala njhalu ngati zimenezo, nikudyelela umoyo waufulu, akhala mnyumba ya mafumu, sakhala mthengo! 26 Nambho, mudapita kuona chiyani? Bwanji, mudapita kumuona mlosi? Yetu, mdapita kumuona mundhu wamkulu kupitilila mlosi. 27 Yohana mmeneyu ndeuyo nghani zake zalembedwa Mmalembo Yoyela,
‘Penya, sinimtume mthenga wanga wakuchogolele,
uyo wakukonjela njila yopita iwe.’ 28 Nikukambilani, pakati pa wandhu wonjhe abalidwa ni wachikazi, palibe uyo wali wamkulu kupitilila Yohana mbatizi. Nambho, uyo wali wamng’ono kwambili pa ufumu wa Mnungu wali wamkulu kupitilila Yohana."
29 Wandhu wonjhe pamojhi ni wolandila malipilo, anyiyawa adabatizidwa ni Yohana, yapo adavela nghani zimenezo adavomela kuti Mnungu ni wabwino. 30 Nambho a Falisayo ni oyaluza mathauko, adakana yayo adakambilidwa ni Mnungu kuti ayachite, yayo yadakonjedwa ndande yawo, adakana kubatizidwa ni Yohana.