Pular para o conteúdo
Publicidade

Matayo 14

Yesu wayenda pa mwamba pa majhi

22 Yesu yapo wamalaila wandhu, wadaakambila oyaluzidwa wake akwele mbwato wa ukulu kuti achogolele kupita kuchijya kwa nyanja ya Galilaya. 23 Yapo wadamaliza kwalaila wandhu, wadakwela kuphili kukapembhela. Wadakhala kumeneko yokha mbaka usiku yapo udajha. 24 Ndhawi imeneyo bwato lalikulu lidafika pakatikati pa nyanja, uku nilindengandenga kwa mafunde ndande mbhepo imalibula.

25 Mmalenga kucha, Yesu wadaachata oyaluzidwa uku niwayenda pa mwamba pa majhi. 26 Oyaluzidwa wake yapo adamwona niwayenda pa mwamba pa majhi, adaopa ni kukamba, "Chimzilimu!" Adabula phokoso ndande ya mandha.

27 Nambho pampajha Yesu wadaakambila, "Jhithileni mtima, ni ine. Msadaopa!"

28 Petulo wadamkambila, "Ambuye, ngati nde imwe, nikambileni nikuchateni pakuyenda pa mwamba pa majhi."

29 Yesu wadamkambila, "Chabwino, majha." Ndiipo Petulo wadachika mbwato waukulu, wadayenda pamwamba pa majhi ni kumpitila Yesu. 30 Petulo yapo wadawona mbhepo yaikulu, wadaopa ni kuyamba kubila uku niwabula phokoso, "Ambuye, nipulumucheni!"

31 Pampajha, Yesu wadatambasula jhanja lake, wadamgwila ni kumkambila, "Iwe wa chikulupi chochepa, ndande yanji uopa?"

32 Ndiipo adakwela mbwato waukulu, ni mbhepo nayonjho idasiya. 33 Wonjhe adali mbwato waukulu, adagwada ni kumkwatamila, niakamba, "Zenedi iwe ni Mwana wa Mnungu."

Veja também