Yesu wang’anamuka nghope
1 Yapo yadapita masiku sita, Yesu wadaatenga Petulo, Yakobo ni Yohana mbale wa Yakobo, wadaatenga anyiiwo okha nikupitanao pa pamalo ya chisisi. 2 Kumeneko, Yesu wadang’anamuka nghope pamaso pawo, nghope yake idali yophulikila ngati jhuwa ni njhalu zake zidali zoyela mbee. 3 Ndiipo, Musa ni Eliya adaatulukila pachogolo pao, adakamba ni Yesu. 4 Ndiipo Petulo wadamkambila Yesu, "Ambuye, siikhale bwino ngati sitikhale pano! Ngati mukonda sinimange visakasa vitatu, chimojhi chanu, chimojhi cha Musa ni chimojhi cha Eliya."
5 Petulo yapo wamakamba chimwecho, mtambo wong’azikila udavinikila, ni mvekelo udaveka kuchoka kumtambo, "Uyu nde Mwana wanga uyo nimkonda, nikondwela nayo kupunda, mveleni iye."