Pular para o conteúdo
Publicidade

Mateus 18

Chifani cha mbowa uyo siwalekelela

21 Ndiipo Petulo wadamchata Yesu ni kumfunjha, "Ambuye, mbale wanga wakanililakwila, nimlekelele kangati? Bwanji, mala saba ikwana?"

22 Yesu wadamuyangha, "Sinikamba mala sabape, nambho saba mala sabini. 23 Ufumu wa kumwamba uli chimwechi, mfumu mmojhi wamafuma kuchita chiwelengelo cha chuma chake iye pamojhi ni mbowa zake. 24 Yapo wadayamba kuwelengecha, mundhu mmojhi uyo wadakongola ndalama miliyoni zambili, wadapelekedwa kwaiye. 25 Pakuti wadalibe chindhu chobweza ngongole, mfumu wake wadalamula kuti iye ni mkazake ni wana wake ni vonjhe ivo wadalinavo vigulichidwe, kuti ibwezedwe ngongole. 26 Mbowa yujha wadamgwadila ni kukamba, Unilengele lisungu, sinibweze ngongole yako yonjhe.27 Mkuluyo wadamlengela lisungu, wadamlekelela ngongole yake ni kumsiya wajhipita."

28 "Nambho mbowa yujha yapo wamatuluka kubwalo wadakomana ni mbowa mnjake uyo wadamkongola ndalama zokwana laki imojhi. Wadamgwila ni kumkhaba pakhosi, niwakamba, Bweza ndalama zanga!29 Mbowa mnjake yujha wadamgwadila ni kumpembha, Nilengele lisungu, sinikubwezele ndalama yako yonjhe.30 Nambho iye wadakana. Wadampeleka kundende mbaka yapo siwabweze ndalamazo. 31 Mbowa wina yapo adaona yayo yadachitika, adadandaula kupunda, nawo adapita kumkambila mfumu wao kila chindhu icho yadachokela. 32 Ndiipo yujha mfumu wadamtana mnyumba yujha mbowa, wadamkambila, Iwe mbowa woipa! Ine nidakulekelela ngongole zako zonjhe ndande udanipembha, ni nidachita chimwecho. 33 Bwanji, iwe siudafunike kumlengela lisungu mnjako, ngati umo nakulengela ine?34 Chimwecho mfumu wake yujha wadakwiya kupunda, wadampeleka kundende mbowa wake yujha kuti wavutike mbaka yapo siwabweze ngongole yonjhe."

35 Yesu wadamaliza pokamba, "Umu ndeumo Atate wanga akumwamba siakuchiteni ngati simwaalekelela achanjanu volakwa vao."

Veja também