37 Kujha kwa Mwana wa Mundhu sikulingane ni chijha chidachokela nyengo ya Nuhu. 38 Pa masiku yameneyo ikali osachokele vula ya ikulu, wandhu amadya ni kumwa, waachimuna ni wachikazi amakwata ni kukwatiwa, mbaka yapo Nuhu wadalowa mkati mwa chombo. 39 Wandhu achameneo siamajhiwe chalichonjhe icho sichichokele. Vula yambili idagwa ni kwaapha wandhu wonjhe. Chimwecho ndeumo siikhalile yapo siwabwele Mwana wa Mundhu. 40 Nyengo imeneyo, waachimuna awili sakhale nialima mmunda, mmojhi siwatengedwe, mwina siwasiidwe. 41 Wachikazi awili siakhale pambhelo naapela chakudya, mmojhi siwatengedwe, mwina siwasiidwe.