Upandu wa kumpha Yesu
1 Yesu yapo wadamaliza kuyaluza yonjhe, wadaakambila oyaluzidwa wake, 2 "Ngati umo mjhiwila kuti pambuyo pa masiku yawili sikukhale pwando la Pasaka, ni Mwana wa Mundhu siwapelekedwe kwa adani wake kuti wapachikidwe pamtanda."
3 Ndiipo ajhukulu wakulu ni wakulu a wandhu adakomana pamojhi mnyumba ya milandhu wa Mjhukulu Wamkulu uyo watanidwa Kayafa, 4 adakambilana upandu wa kumgwilila Yesu kwa chisisi kuti amphe. 5 Anyiiwo adakambilana, "Siifunika tichite chimwechi ndhawi ya phwando la Pasaka, wamdhu siadachita mkanganjili pakati pa wandhu."
Yesu wapungulilidwa mafuta ku mujhi wa Besania
6 Yesu wadali ku Besania mnyumba mwa Simoni uyo wadali ni makate. 7 Yesu yapo wamadya, wadajha wamkazi mmojhi uyo wadasenjhela njhupa ya mafuta yonunghila ya mtengo waukulu, wadayapungulila pamutu pa Yesu. 8 Oyaluzidwa wake yapo adaona chimwecho adakwiya, adafunjhana, "Ndande chiani wayawananga chimwechi mafuta yaya? 9 Mafuta yonunghila yaya yadakakhoza kugulichidwa kwa mtengo waukulu ni ndalama kwaapacha osauka!"
10 Yesu wadajhiwa icho amakamba, wadaakambila, "Ndande yanji mumchaucha wamkaziyu? Uyu wamkazi wanichitila chindhu chabwino kupunda. 11 Osauka simukhale nawo masiku yonjhe, nambho ine simukhala nane masiku yonjhe. 12 Yapo wanipungulila mafuta yaya pathupi, wachita chimwecho dala kukonjekela kuzikidwa kwanga. 13 Zenedi nikukambilani, kulikonjhe uko kulalikidwa uthenga wabwino, chindhu ichi wachichita wamkazi huyu sichilalikilidwe kwa kumkumbukila iye."
Yuda wavomela kumng’anamuka Yesu
14 Ndiipo mmojhi wa anyiwajha oyaluzidwa khumi ni awili, uyo wamatanidwa Yuda isikaliote wadapita kwa wakulu a jhukulu, 15 wadaafunjha, "Simunipache ndalama zingati nikamng’anamuka Yesu kwanu?" Chimwecho adamuwelengela magelenjha selasini ni kumpacha. 16 Kuyambila pamenepo Yuda wamafunafuna mtundu wabwino wa kumng’anamuka Yesu.
Yesu wakudya chakudya cha Pasaka pamojhi ni oyaluzidwa wake
17 Msiku loyamba la pwando la mabumunda yayo yalibe amila, oyaluzidwa adajha kwa Yesu ni kumfunjha, "Ufuna tikakukonjekele kuti chakudya cha pwando la Pasaka?"
18 Yesu wadaayangha, "Pitani mmujhi kwa wammuna mmojhi, mukamkambile, ‘Oyaluza akamba, saa yanga yafika, ine ni oyaluzidwa wanga sitidye chakudya cha Pasaka mnyumba yako.’ "
19 Oyaluzidwa adachita ngati umo Yesu wadaakambila, adakonja chakudya cha pwando la Pasaka.
20 Yapo udafika ujhulo, Yesu ni oyaluzidwa wake khumi ni awili adakhala kudya chakudya. 21 Yapo amadya, Yesu wadaakambila, "Zenedi nikukambilani, mmojhi wanu siwaning’anamuke."
22 Oyaluzidwa wake adavachisoni kupunda, adayamba kumfunjha mmojhimmojhi, "Ambuye, bwanji, ni ine?"
23 Yesu wadayangha, "Mundhu mmojhi uyo wasunjha bumunda lake mmbale pamojhi ni ine, nde uyo siwaning’anamuke. 24 Mwana wa Mundhu siwamwalile ngati mujha idalembeledwela mu malembo. Nambho siwavutike mundhu yujha wamng’anamuka Mwana wa Mundhu! Idakakhala mbasa kwa mundhu mmeneyo kuti siwadakabadwa."
25 Ndiipo Yuda, yujha wamng’anamuka, wadakamba, "Oyaluza, nde ine kani?"
Yesu wadamuyangha, "Yetu, nde iwe ngati umo wakambila."
Chakudya cha Ambuye
26 Yapo amadya Yesu wadatenga bumunda, wadayamika, wadaubandhula, ni kwapacha oyaluzidwa wake nikukamba, "Tengani mudye, ili nithupi langa."
27 Ndiipo wadatenga chikho, wadayamika Mnungu, ni kwaapacha oyaluzidwa wake niwakamba, "Mwaonjhe mchimwele chikho ichi, 28 uwu nde mwazi wanga uwo uchimikiza chipangano, umwazika ndande ya ambili dala machimo yao yalekeleledwe.