Yesu wapembhela ku busitani ya Getisemane
36 Ndiipo Yesu wadapita pamojhi ni oyaluzidwa wake pa malo yapo pamatanidwa Getisemani, ni iye wadaakambila, "Khalani pano ine nipite yapo kukapembhela."
37 Wadatenga Petulo ni wana awili Azebedayo, wadayamba kuva chizoni ni kulaga mumtima. 38 Kumeneko wadaakambila, "Nili ni chisoni chachikulu mumtima mwanga icho chikhoza kunipha. Khalani pano ni muchezele pamojhi ni ine."
39 Wadapita pachogolo pang’ono, wadagwa panjhi chifufumimba ni kupembhela, "Atate wanga, ngati ikhozeka, nichocheleni chikho ichi cha mavuto! Chipano osati ngati umo nifunila ine, nambho ngati umo mufunila imwe."
40 Ndiipo wadabwela kwa oyaluzidwa wake ni kwaapheza agona, wadamkambila Petulo, "Ikhala bwanji simdakhoze kuchezelela ni ine ata kwa saa imojhipe? 41 Chezelani ni kupembhela kuti msadalowa mu mayeselo. Mtima ufuna kuchita yayo yafunika, nambho thupi lilibe mbhavu."
42 Wadapitanjho kakawili wadapembhela, "Atate wanga, ngati siikhozeka kuchichocha chikho ichi chamavuto, basi mchite umo mfunila." 43 Yapo wadabwela kakawili wadaaphezanjho agonanjho ndande maso yao yadali ni litulo.
44 Chimwecho wadaasiyanjho ni kupita kupembhela kakatatu ni wakamba mau yamweyajha. 45 Ndiipo wadabwela kwa oyaluzidwa wake ni kwakambila, "Bwanji, mkali kugona ni kupumulila? Vechelani, saa yakwana Mwana wa Mundhu siwagwilidwe ni wandhu amachimo. 46 Imani tijhipita. Yujha waning’anamuka watokujha."