Pular para o conteúdo
Publicidade

Mateus 5

Kwakonda adani

43 "Mwavela kuti idakambidwa kuti, Mkonde mnjako ni umuipile mdani wako.44 Nambho ine nikukambilani akondeni adani wanu ni kwapembhela anyiyao akuvutichani anyiimwe, 45 kuti mkhale wana wa Atate wanu ali kumwamba. Pakuti iye wawalichila jhuwa lake wandhu woipa ni wandhu abwino ni kwanyechela vula wandhu yawo achita ivo vivomelezeka kwa Mnungu ni wandhu yawo saachita vovomelezeka. 46 Bwanji, simupate chikho chanji ngati simwaakonde wajha akukondanipe? Palibe! Pakuti olandila malipilo nawo achita chimwecho. 47 Chinchijha ngati mkaalonjela abale wanupe bwanji, mchita chindhu chanji chachikulu kupitilila wandhu wina? Ata wandhu yawo samjhiwa Mnungu saachita chimwecho. 48 Chimwecho khalani wokwanila ngati Tate wanu wa kumwamba umo wali okwanila."

Veja também