7 Nambho nikukambilani uzene, mbasa ine nipite, mate yake nikasiya kupita Othandiza siwajha kwanu. Nambho nikapita, sinimtume kwanu. 8 Nayo yapo siwajhe siwachimikizile wandhu ajhiko nghani za machimo, kuvomelezeka ni lamulo la Amnungu. 9 Achita machimo, ndande sanikhulupilila, 10 Mzimu woyela siwachimikizile kuusu kuvomelezeka kwanga pachogolo pa Amnungu, ndande nipita kwa Atate, nawo sanionanjho. 11 Kuusu kulamula, ndande satana wamkulu wa jhiko lino, watho lamulidwa.