13 Nambho mtumiki wa kumwamba wa Mnungu wadamkambila, "Zakaliya Usadaopa, pakuti Mnungu wavela mapembhelo yako, ni mkazako Elizabeti siwakubalile mwana wammuna, ni iwe siumpache jhina Yohana. 14 Nawe siusekelele ni kukondwela kupunda, ni wandhu ambili sakondwele chifuko cha kubadwa kwake. 15 Ambuye samchite kukhala wamkulu, ni siwamwa divayi kapina chakumwa chilichonjhe cholojhelecha, siwajhazidwe ni Mzimu Woyela kuyambila siku lakubadwa kwake. 16 Yohana siwaabweze wandhu ambili Akuizilaeli kuti abwele kwa Ambuye Mnungu wao. 17 Ni iye siwachogolele pachogolo pa Ambuye ni siwachogozedwe ni mzimu ni mbhavu ngati za Eliya. Siwaing’anamuche mitima ya achatate kuti yaaganizile achanawao, ni kwachita osavela kuti akhale ni maganizo yabwino, ni kwaika wandhu wake tayali pakujha kwa Ambuye."