34 Maliya wadamuyangha ni kumfunjha mtumiki wa kumwamba wa Mnungu, "Sivikhozekane bwanji vindhu ivi, pakuti sinidapezane chithupi ni wammuna?" 35 Mtumiki wa kumwamba wa Mnungu wadamuyangha Maliya, "Mzimu woyela siukujhele iwe, ni mphavu zake uyo wali kumwamba kupunda sizikuvinikile iwe ngati chitunjhi. Chimwecho, ni Woyela uyo siwabadwe siwatanidwe Mwana wa Mnungu.