Pular para o conteúdo
Publicidade

Lucas 1

Ulosi wa Zakaliya

67 Ndiipo Zakaliya, tate wa Yohana wadajhazidwa ni Mzimu Woyela, ni wadakamba ulosi,

68 "Akwezedwe Ambuye Mnungu aku Izilaeli,

pakuti wajha kwaombola wandhu wake.

69 Iye watipacha muomboli wambhavu,

Wochokela mbadwa wa Daudi mbowa wake.

70 Ngati umo Mnungu wadakamba kuyambila kale,

kupitila alosi wake woyela,

71 kuti siwatilamiche ife kuchokela kwa adani

ni kuchokela mmanja mwa wandhu yawo atiipila ife.

72 Wadakamba kuti siwachitile ubwino achambuyathu,

ni kukumbukila chipangano chake choyela.

73 Ngati umo wadamuahidi tate wathu Ibulahimu kwa kulumbila,

kuti siwatipache ife mwawi,

74 Siwatichoche ife mmanja mwa adani wathu,

watikhozeche kumtumikila iye popande mandha,

75 moyela ni kuvomelezeka pamaso pa Mnungu,

masiku yonjhe ya umoyo wathu.

76 Ni iwe mwana wanga siutanidwe mlosi wa uyo wali kumwamba kupunda.

siwachogolele Ambuye kwakonjela njila yao,

77 ni siwauzile wandhu wao kuti sialamichidwe

kwa njila ya kwalekelela machimo yao.

78 Ndande ya lisungu ni upole wa Mnungu wathu,

ni dangalila la kulamicha kwake sikutiwalile kuchokela kumwamba,

79 kuti lamulikile wandhu wojhe yawo akhala kumdima waukukulu wa nyifa,

nikutichogoza munjila ya mtendele."

Veja também