15 Ndiipo Yesu wadaakambila wandhu wajha, "Mujhipenyelele ni chipili vindhu vonjhe, pakuti umoyo wa mundhu siupatikana ndande ya kuchuluka kwa chuma icho walinacho mundhu." 16 Ndiipo Yesu wadapacha chifani, "Kudali ni wopata mmojhi uyo wadali ni munda uwo udabala vipacho vochuluka. 17 Mundhu wopata mmeneyo wadayamba kuganizila mumtima mwake, ‘Nichite chiyani? Pakuti nilibe malo yosungila chakudya changa icho nachikolola. 18 Sinigomole nghokwe zanga ni kumanganjho zazikulu kupitilila ni mmenemo, nde umo siniikemo vokolola vanga vonjhe ni chuma changa.’ 19 Pamenepo siniukambile mzimu wanga, ‘Chipano uli ni chuma cha mbili, ivo udavisunga kwa vyaka vambili. Pumulila, udye, umwe ni kukondwela.’ 20 Nambho Mnungu wadamkambila, ‘Wopusa iwe! Umoyo wako siutengedwe usiku uno. Ni vindhu vonjhe ivo wajhiunjikila sivikhale vayani?’"
21 Yesu wadakamba, "Umu nde umo ili kwa yawo ajhiunjikila chuma cha mbili mwene wake, nambho alibe chindhu icho chili chokhadwa pamaso pa Mnungu."