Yesu wamulamicha wamkazi siku Lopumulila Ayahudi
10 Siku limojhi Lopumulila, Yesu wamatoyaluza mnyumba yopembhelela Ayahudi. 11 Mnyumba mmenemo mudali wamkazi mmojhi uyo wamalamulidwa nichiwanda pavyaka khumi ni nane. Nayo wadali nichipindi, nisiwamakhoze kuima. 12 Yesu yapowadamwona wamakazi mmeneyo, wadamtana, ni wadamkambila, "Wamkazi, wamasulidwa chipindi chako." 13 Yesu yapo wadamwikila manja pamwamba pa mutu wake kwa kughafya, ghafula thupi lake lidakhululukanjho, wadayamba kumtamanda Mnungu. 14 Nambho wamkulu wa nyumba ya mapembhelo wadakwiya ndande Yesu wadamlamicha wamkaziyo siku lo pumulila. Nde wamkulu wa nyumba yopezelana ayahudi wadakambila wajha wandhu, "Mulinisiku sita izo mfunika kuchita njhito. Chipano, mjhijha pasiku zimenezo kulamichidwa, nambho osati siku Lopumulila." 15 Ndiipo Yesu wadayangha, "Aghunguli anyimwe! Bwanji, palije uyo wamasulila punda kapina ng’ombe wake kuchokela mkhola nikupita nayo kumwechela majhi ata ngati siku Lopumulila? 16 Ni uyu wamkazi uyu, uyo wali mbadwa wa Ibulahimu, wavutichidwa ni Satana kwa vyaka kumi ni nane. Bwanji, siwafunika kulamichidwa ata ngati siku Lopumulila?" 17 Yapo wadamaliza kukamba chimwecho, adani wonjhe wake adalenga mwano, nambho wandhu adakondwa kupunda ndande ya vodabwicha ivo wadachita Yesu.