20 Ndiipo wadayamba ulendo wopita kwa atate wake. Nambho yapo wadali wakali patali, atate wake adamuona, adamlengela lisungu. Adamthamangila mwana wao ni kumkhumbatila kwa chisangalalo. 21 Mwana yujha wadaakambila atate wake, ‘Atate, nakuchimwilani imwe ni Mnungu. Sinifunikanjho kutanidwa mwana wanu.’ 22 Nambho atate wake adaakambila mbowa zake, ‘Pita chisanga katenge njhalu yabwino mumveke! Mvekeni pete ni malapasi ya mtengo waukulu! 23 Mkamtenge njinda ya ng’ombe wonona tichinje, tichite phwando ni tidye!