29 Yesu wadamkambila, "Chabwino, majha." Ndiipo Petulo wadachika mbwato waukulu, wadayenda pamwamba pa majhi ni kumpitila Yesu. 30 Petulo yapo wadawona mbhepo yaikulu, wadaopa ni kuyamba kubila uku niwabula phokoso, "Ambuye, nipulumucheni!"
31 Pampajha, Yesu wadatambasula jhanja lake, wadamgwila ni kumkambila, "Iwe wa chikulupi chochepa, ndande yanji uopa?"