Ochita njhito mmunda wa mizabibu
1 "Ufumu wa kumwamba ulingana ni mwene munda uyo wadachoka umawawa, wadapita kwaafunafuna wandhu akachite njhito mmunda wake wa mizabibu. 2 Wadavomela kwaalipa ndalama ya njhito ya siku limojhi, ndiipo wadaapeleka mmunda mwake akachite njhito. 3 Pambuyo pa masaa yatatu umawa, wadaapheza wandhu wina aima pamalo yokomanilana wandhu ni alibe njhito. 4 Wadaamkambila, ‘Anyiimwe namwenjho mapitani mukachite njhito kumunda wanga wa zabibu, nane sinikulipeni mkokolo wanu ngati umo ifunikila.’ 5 Ndiipo adapita pamojhi. Mwene munda yujha wadachokanjho saa sita ni saa tisa, wadachita chinchijha ngati umo wadachitila poyamba. 6 Yapo idakwana saa khumi namojha ujhulo, wadachokanjho ni kukomana ni wandhu wina aima pamalo yogulichila malonda. Basi, wadaafunjha, ‘Ndandeyanji mwaima pano usana wonjhewu popande njhito?’ 7 Anyiiwo adamuyangha, ‘Palibe uyo watupacha njhito,’ Nayo wadaakambila, ‘Anyiimwe namwenjho pitani mkachite njhito ku munda wanga wa zabibu.’
8 "Ujhulo yapo udafika, mwene munda yujha wadamkambila woimilila wake, ‘Atane ochita njhito waalipe ndalama zao, uyambe ni othela ndiipo achate wajha adachogolela kuchita njhito.’ 9 Wandhu adachita njhito kuyambila saa khumi na mojha, kila mmojhi wadalipidwa mkokolo wake wa siku limojhi. 10 Anyiwajha adachogolela kuchita njhito yapo adajha, amaganiza kuti saapachidwe papakulu, nambho naonjho adalandila kila mmojhi mkokolo umweujha wa siku limojhi. 11 Yapo adalandila mkokolo wao, adayamba kumdandaulila yujha mwene munda. 12 Adakamba, ‘Anyiyawa achita njhito mmathelo, achita njhito kwa saa imojhipe, ndandeyanji alandila mkokolo wolingana ni ife, tachita njhito siku lambhumbhu pajhuwa?’ 13 Pamenepo yujha mwene munda wadamuyangha mmojhi wao, ‘Bwenji langa, sinidakuchefye. Bwanji, sitidavomelezane kukupachani mkokolo wa siku limojhi? 14 Tenga chili chako ujhipita. Nifuna kumpacha uyu wothela ngati umo nakupachila iwe. 15 Bwanji, osati bwino ine kuchita icho nifuna kuchita kwa ndalama zanga? Bwanji, kapina uwona njhanje ndande ine nili ni mtima wabwino?’"
16 Yesu wadamalizila pokamba, "Chimwecho wothela siwakhale oyamba ni woyamba siwakhale wothela."