Yesu wamlamicha mbowa wa mkulu wa loma
5 Yesu yapo wadalowa ku Kapelinaumu, wamkulu wa gulu la asilikali mmojhi wa kuloma, wadamchata ni wadampembha wamthangatile. 6 Ndiipo wadakamba, "Imwe Ambuye, mbowa wanga wagona kukhomo, wavuwala ni wadwala kupunda."
7 Yesu wadamkambila, "Sinijhe kumlamicha."
8 Nambho yujha wamkulu waloma wadamkambila, "Imwe Ambuye, ine sinifunika imwe mulowe mnyumba mwanga, nambho chochani lamulope, ni mbowa wanga siwalame. 9 Pakuti ata ine nichogozedwa ni waakuluakulu wina, nilinawo asikali yao naachogoza. Nimlamula mmojhi, ‘Pita!’ Nayo wapita, ‘Majha!’ Nayo wakujha ni mbowa wanga, ‘Chita chindhu ichi! Nayo wachita.’ "
10 Yesu yapo wadavela chimwecho, wadazizwa, wadaakambila wandhu wajha adamchata, "Zene nikukambilani, sinidaone mundhu waliyonjhe mujhiko la Izilaeli uyo wali ni chikhulupi ngati ichi. 11 Zenedi nikukambilani, wandhu ambili siajhe kuchokela dela la kumwela ni kumpoto, nawo siakhale papwando pamojhi ni Ibulahimu ni Isaka ni Yakobo pa ufumu wa kumwamba. 12 Nambho wajha amafunika kukhala mu ufumu wa Mnungu saataidwe kubwalo mumdima, uko sikukhale chililo ni kukukuta mano." 13 Ndiipo Yesu wadamkambila yujha wamkulu wa Loma, "Pita kukhomo, ni ikhale ngati umo wakhulupilila."
Ni mbowa wake wadalama saa imweijha.