13 Nambho mtumiki wa kumwamba wa Mnungu wadamkambila, "Zakaliya Usadaopa, pakuti Mnungu wavela mapembhelo yako, ni mkazako Elizabeti siwakubalile mwana wammuna, ni iwe siumpache jhina Yohana. 14 Nawe siusekelele ni kukondwela kupunda, ni wandhu ambili sakondwele chifuko cha kubadwa kwake. 15 Ambuye samchite kukhala wamkulu, ni siwamwa divayi kapina chakumwa chilichonjhe cholojhelecha, siwajhazidwe ni Mzimu Woyela kuyambila siku lakubadwa kwake.