14 Yesu yapo wadaaona amakate wajha, wadaakambila, "Pitani mkajhilangize kwa ajhukulu." Yapo adali akali mnjila, adalama utenda ni kuvomelezeka kwa chikhalidwe cha kumlambila Mnungu. 15 Mmojhi wao yapo wadaona kuti walama, wadabwelela kwa Yesu uku niwamtamanda Mnungu kwa mvekelo waukulu. 16 Wadagwa chifufumimba mmiyendo ya Yesu ni kumuyamika. Mundhu mmeneyo wadali Msamaliya. 17 Yesu wadamfunjha, "Bwanji, osati wandhu khumi yao adalamichidwa ni kuvomelezeka kwa chikhalidwe cha kumlimbila Mnungu? Bwanji, anyiwajha tisa alikuti? 18 Bwanji, padalibe ata mmojhi uyo wadabwela kumpacha ulemu Mnungu, nambho uyu mlendope?" 19 Ndiipo Yesu wadamkambila mundhu yujha, "Ima ujhipita, chikhulupililo chako chakulamicha."