Pular para o conteúdo
Publicidade

Lucas 24

Yesu watulukila awili mnjila ya Emau

13 Siku limwelo aochatila wake awili adali paulendo wopita ku muchijhijhi chimojhi icho chimatanidwa Emau. Utali wake ni wokwana kilometa kumi ni imojhi kuchokela ku Yelusalemu. 14 Anyiiwo amakambilila vindhu ivo vachokela. 15 Yapo adali akali niakamba ni kukambilana kuusu ngani zimenezo, Yesu mwenewake wadatulukila ni kuyenda pamojhi na anyiiwo. 16 Adamuona ni maso yawo, nambho adachekelezedwa kuti siadakhoza kumjhiwa.

17 Yesu wadaafunjha, "Bwanji, nghani zanji izo mkambilana uku ni muyenda?" Wandhu wajha adaima uku ali chete, nghope zao nizilangiza chisoni. 18 Mmojhi wao uyo wamatanidwa Kileopa wadamfunjha, "Bwanji, iwe ni mlendo kuno ku Yelusalemu mbaka usadajhiwa vindhu ivo vachokela pamasiku yochepaya?" 19 Yesu wadafunjha, "Vindhu vanji ivo vachokela?" Adamuyangha, "Nghani za Yesu waku Nazaleti. Iye wadali mlosi, wa mbhavu pa ivo wamavichita ni pakukamba kwake, pachogolo pa Mnungu ni pachogolo pa wandhu wonjhe. 20 Ajhukulu wa akuluakulu ni achogoleli awandhu adamchocha kuti walamulidwe nyifa, ni anyiiwo adampachika pamtanda. 21 Nambho ife timakhulupilila kuti iye nde uyo wadatumidwa kwaombola wandhu a Izilaeli. Kupitilila yameneyo, lelo ni siku la katatu kuyambila vachitika vimenevi. 22 Ni wachikazi wina pagulu lathu atizizwicha. Adapita pachiliza lelo umawamawa, 23 nambho sadachikomane chitanda cha Yesu. Adabwelela ni kukamba kuti atulukilidwa ni atumiki akumwamba Amnungu, yawo adakambila kuti Yesu wakali wamoyo. 24 Wandhu wina yawo adali pamojhi ni ife, adapita pachiliza kukaona yayo adakambilidwa ni wachikazi wajha, nambho sadamkomane Yesu."

25 Ndiipo Yesu wadakambila, "Wandhu anyiimwe ni asabobwa kupunda. Niwolimba kukhulupilila icho chidalamebdwa ni alosi? 26 Bwanji, siidafunike Kilisito uyo wasanghidwa ni Mnungu wavutike ni walowe mu ulemelelo wake?" 27 Yesu wadafotokozela umo malembo yonjhe umo yakambila kuusu iye, kuyambila malembo ya Musa mbaka malembo ya alosi wina wonjhe.

28 Yapo adawandikila pa mujhi uwo amapita, Yesu wadajhichita ngati wayendekela ni ulendo. 29 Nambho anyiiwo adampembelela Yesu, niakamba, "Ukhale ni ife pakuti chipano ni ujhulo ni usiku wathowandikila." Ndiipo wadolowa mnyumba ni kukhala nawo. 30 Yapo wadakhala kudya chakudya pamojhi ni anyiiwo, iye wadatenga bumunda ni kwayamika Amnungu, wadaubandhula nikwaapacha. 31 Ndhawi imweyo maso yawo yadamasuka, adamjhiwa kuti ni Yesu, ni iye wadasowa pakati pawo. 32 Ndiipo adafunjhana, "Bwanji, mitima yathu siimakwelele kwa kukondwela yapo wamakamba niife ni kutifotokozela malembo mnjila mujha?" 33 Ndhawi imweyo adachoka ni kubwela ku Yelusalemu. Kumeneko adakomana anyiwajha atumwi khumi ni mmojhi ni wandhu anyiyawo adali pamojhi ni anyiiwo, 34 adakamba, "Zenedi, Ambuye ahyuka ni wamtulukila Simoni." 35 Ndiipo, wajha awili wadafotokozela achanjawo yayo yadachokela kunjila ni umo adamjhiwila Yesu, yapo wadabandhula bumunda.

Veja também