Chifani cha chindhu cha phindhu lalikulu chabisidwa
44 "Ufumu wa kumwamba ulingana ni chindhu cha phindu icho chabisidwa mmunda. Mundhu mmojhi wadachivumbula, wadachibisanjho, ni kukondwela kwa kukulu uko wadali nako, wadapita kugulicha vonjhe ivo wadalinavo, ndiipo wadabwela kugula munda ujha."
Chifani cha mwala wa phindhu uwo utanidwa lulu
45 "Ufumu wa kumwamba ulingana ni wochita malonda mmojhi uyo wamafunafuna lulu ya bwino. 46 Yapo wadapeza lulu imojhi ya phindu lalikulu, wadapita kugulicha vonjhe ivo wadalinacho ni kugula lulu ijha."