Yesu wakambilila kugomoledwa kwa nyumba ya Mnungu
1 Yesu yapo wadatuluka kubwalo kwa nyumba ya Mnungu, yapo wamachoka oyaluzidwa wake adampitila ni adayamba kukamba naye kuusu nyumba ya Mnungu. 2 Yesu wadafujha, "Bwanji, muzipenya izi zonjhe? Zene nikukambilani, palibe ata mwala umojhi uwo siukhalile pamwamba pa wina, kila mwala siugwechedwe panjhi."