Kujha kwa Mwana wa Mundhu
29 "Yakathokutha mavuto ya masiku yameneyo, jhuwa silithilidwe mdima, ni mwezi siung’azikila, ndhondwa sizigwe kuchoka ku mlengalenga, ni mbhavu za kumlengalenga sizitingizidwe. 30 Ndiipo sipachokele chizindikilo cha Mwana wa Mundhu kumlengalenga ni mafuko yonjhe ya pajhiko siyaimbe nyimbo za zaya. Nawo siamuone Mwana wa Mundhu niwajha pamwamba pamitambo ya kumlengalenga, mu mbhavu ni ulemelelo waukulu. 31 Mbetete zazikulu sizipulizidwe, ni iye siwaatume atumiki wake akumwamba ku njhonga zinayi za jhiko lapanjhi. Anyiiwo saike pamojhi wandhu wake yawo asanghidwa kuyambila dela limojhi la jhiko mbaka kudela lina."