14 "Anyiimwe ni dangalila la jhiko! Ni ngati nyumba iyo yamangidwa pamwamba pa phili siukhoza kubisika. 15 Wandhu saakweleza nyali ni kuikupika kwa debe. Nambho iyikidwa pamwamba poikila nyali kuti imulikile wandhu wonjhe yao ali mnyumba. 16 Chimwecho dangalila lanu liwale pamaso pa wandhu kuti apenye vichito vanu vabwino ni kwaakweza Atate wanu akumwamba."